Song of Solomon 8:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo, atatsamira wokondedwa wake? Mkazi Ndidakudzutsa patsinde pa mtengo wa apulosi uja. Pamenepo mpamene amai ako adachirira pokubala iweyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndaniyu achokera kuchipululu, alikutsamira bwenzi lake? Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe: Pomwepo amai ako anali mkusauka nawe, pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo, atatsamira wokondedwa wakeyo? Ndinakudzutsa pa tsinde pa mtengo wa apulosi, pamenepo ndi pamene amayi anachirira, pamenepo ndi pamene wokubereka anamva ululu pokubala iweyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndaniyu acokera kucipululu, Alikutsamira bwenzi lace? Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe: Pomwepo amako anali mkusauka nawe, Pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe.