Song of Solomon 8:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Umatirire mtima wako kuti musaloŵe winanso koma ine ndekha, ndipo sudzakumbatira winanso koma ine ndekha. Paja chikondi nchamphamvu ngati imfa, nsanje njaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti laŵilaŵi ngati malaŵi a moto, ndipo nchotentha koopsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro, nundikhomenso chizindikiro pamkono pako; pakuti chikondi chilimba ngati imfa; njiru imangouma ngati manda: Kung'anima kwake ndi kung'anima kwa moto, ngati mphezi ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Undiyike pamtima pako ngati chidindo, ngati chidindo cha pa dzanja lako; pakuti chikondi nʼchamphamvu ngati imfa, nsanje ndiyaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti lawilawi ngati malawi a moto wamphamvu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Undilembe pamtima pako, mokhoma cizindikilo, nundikhomenso cizindikilo pamkono pako; Pakuti cikondi cilimba ngati imfa; Njiru imangouma ngati manda: Kung'anima kwace ndi kung'anima kwa moto, Ngati mphezi ya Yehova,