Titus 1:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nkofunika kuŵakhalitsa chete, chifukwa akusokoneza mabanja ena athunthu pakuŵaphunzitsa zimene sayenera kuŵaphunzitsa. Amangochita zimenezi ndi cholinga choipa, chofuna kupata ndalama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja banja lonse, ndi kuphunzitsa zosayenera chifukwa cha chisiriro chonyansa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ayenera kuletsedwa kuyankhula chifukwa akusokoneza mabanja athunthu pophunzitsa zinthu zomwe sayenera kuwaphunzitsa. Iwo amachita izi kuti apeze ndalama mwachinyengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja banja lonse, ndi kuphunzitsa zosayenera cifukwa ca cisiriro conyansa.