Titus 1:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwa anthu oyera mtima, zinthu zonse nzoyera. Koma kwa amene ali odetsedwa ndi osakhulupirira, palibe kanthu koyera; mitima yao ndi nzeru zao zomwe, zonse nzodetsedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupirira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi chikumbu mtima chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa oyera mtima, zinthu zonse ndi zoyera, koma kwa amene ndi odetsedwa ndi osakhulupirira, palibe kanthu koyera. Kunena zoona, mitima yawo ndi chikumbumtima chawo, zonse nʼzodetsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi cikumbu mtima cao.