Titus 1:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene zinali zisanalongosokebe, ndi kuti uike akulu a mpingo mu mzinda uliwonse, monga momwe ndidakulamulira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha ichi ndinakusiya iwe m'Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akulu m'midzi yonse, monga ndinakulamulira;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene ndinazisiya zisanathe ndiponso usankhe akulu ampingo mʼmizinda yonse, monga momwe ndinakulamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca ici ndinakusiya iwe m'Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akuru m'midzi yonse, monga ndinakulamulira;