Titus 1:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkulu wa mpingo akhale munthu wosapalamula konse, ndipo akhale wa mkazi mmodzi yekha. Ana ake akhalenso okhulupirira Khristu, opanda mbiri yoti ngosakaza kapena yoti ngosaweruzika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ngati wina ali wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zake, kapena wosakana kumvera mau.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkulu wampingo akhale munthu wopanda cholakwa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, munthu amene ana ake ndi okhulupirira, osati amakhalidwe oyipa ndi osamvera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ngati wina ali wopanda cirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zace, kapena wosakana kumvera mau.