Titus 1:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Woyang'anira mpingo azikhala wosapalamula konse, chifukwa ali ngati kapitao m'banja la Mulungu. Asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena chidakwa, kapena wandeu, kapenanso wokonda kudya phindu la ndalama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda chilema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati wachiwawa, wopanda ndeu, wosati wa chisiriro chonyansa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza mkulu wa mpingo amayendetsa ntchito za banja la Mulungu, ayenera kukhala wopanda cholakwa, asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena womwa zoledzeretsa, kapena wandewu, kapena wopeza phindu mwachinyengo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda cirema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati waciwawa, wopanda ndeu, wosati wa cisiriro conyansa;