Titus 3:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikadzamtuma Aritema kapena Tikiko kwanuko, uchite chotheka kudzandipeza ku Nikopoli, chifukwa ndatsimikiza kuti ndikakhala kumeneko nyengo yachisanu ikubwerayi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene ndikatuma Aritema kwa iwe, kapena Tikiko, chita changu kudza kwa ine ku Nikopoli: pakuti ndatsimikiza mtima kugonerako nyengo yachisanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikadzamutuma Artema kapena Tukiko kwanuko, udzayesetse kundipeza ku Nikapoli, chifukwa ndatsimikiza kukhala kumeneko pa nthawi yozizira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene ndikatuma Artema kwa iwe, kapena Tukiko, cita cangu kudza kwa ine ku Nikopoli: pakuti ndatsimikiza mtima kugonerako nyengo yacisanu.