Titus 3:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse amene ali nane kuno akuti moni. Uperekeko moni kwa onse amene amatikonda chifukwa cha chikhulupiriro. Mulungu akukomereni mtima nonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akukupatsa moni onse akukhala pamodzi ndi ine. Pereka moni kwa otikondawo m'chikhulupiriro. Chisomo chikhale ndi inu nonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse amene ali ndi ine akupereka moni. Upereke moni kwa amene amatikonda ife mʼchikhulupiriro. Chisomo chikhale ndi inu nonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akulankhula iwe onse akukhala pamodzi ndi ine. Lankhula otikondawo m'cikhulupiriro. Cisomo cikhale ndi inu nonse.