Zechariah 1:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo onsewo anauza mngelo wa Chauta amene anaima pakati pa timitengo tazitsamba uja, kuti, ‘Tayendera dziko lapansi, ndipo anthu onse ali pa mtendere, akupumula.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo anamyankha mthenga wa Yehova wakuima pakati pa mitengo yamchisu, nati, Tayendayenda m'dziko, ndipo taonani, dziko lonse likhala chete, lipumula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo okwera pa akavalo enawo anafotokoza kwa mngelo wa Yehova, amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu kuti, “Ife tayendera dziko lonse lapansi ndipo tapeza kuti dziko lonselo lili pa bata ndi mtendere.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo anamyankha mthenga wa Yehova wakuima pakati pa mitengo yamcisu, nati, Tayendayenda m'dziko, ndipo taonani, dziko lonse likhala cete, lipumula.