Zechariah 1:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mngelo wa Chautayo anafunsa kuti, ‘Inu Chauta Wamphamvuzonse, kodi Yerusalemu ndi mizinda ya ku Yuda imene mudaikwiyira pa zaka makumi asanu ndi aŵiri, mudzakhalabe oiwumira mtima mpaka liti?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osachitira chifundo Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mngelo wa Yehova anati, “Yehova Wamphamvuzonse, kodi mpaka liti mudzakhala osaonetsa chifundo chanu kwa Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda, amene mwawakwiyira kwa zaka izi 70?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mthenga wa Yehova anayankha nati, Yehova wa makamu, mudzakhala mpaka liti osacitira cifundo Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, imene munakwiya nayo zaka izi makumi asanu ndi awiri?