Zechariah 1:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ulengezenso kuti Chauta Wamphamvuzonse akuti, “M'mizinda yangayi mudzakhalanso chuma chambiri. Ndidzasangalatsanso Ziyoni, ndipo Yerusalemu ndidzamsandutsanso mzinda wanga wapamtima.” ’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Fuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Midzi yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Lengezanso kuti, Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Mizinda yanga idzakhalanso ndi zokoma zosefukira ndipo Yehova adzatonthoza Ziyoni ndi kusankhanso Yerusalemu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pfuulanso, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu: Midzi yanga idzalemerera ndi kufalikiranso; ndipo Yehova adzasangalatsanso Ziyoni, nadzasankhamo Yerusalemu.