Zechariah 1:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidafunsa mngelo amene ankalankhula nane tanthauzo lake la nyanga zimenezo. Iye adandiyankha kuti, ‘Zimenezi ndizo mphamvu zapansi pano zimene zidabalalitsa anthu a ku Yuda, a ku Israele ndi a ku Yerusalemu.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Izi nziyani? Ndipo anandiyankha, Izi ndi nyangazi zinabalalitsa Yuda, Israele, ndi Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinamufunsa mngelo amene amayankhula nane kuti, “Kodi zimenezi ndi chiyani?” Iye anandiyankha kuti, “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, Israeli ndi Yerusalemu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinati kwa mthenga wakulankhula ndi ine, Izi nziani? Ndipo anandiyankha, Izi ndi nyangazi zinabalalitsa Yuda, Israyeli, ndi Yerusalemu.