Zechariah 1:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidafunsa kuti, ‘Kodi akudzachita chiyani?’ Iye adayankha kuti, ‘Mphamvu zijazi zidabalalitsa Yuda ndi Yerusalemu kotheratu, kotero kuti panalibe ndi mmodzi yemwe woŵeramutsa mutu. Koma amisiri osulaŵa, abwera kudzaopsa ndi kudzaononga mphamvu za mitundu ya anthu imene idaagonjetsa dziko la Yuda, ndi kumwaza anthu ake.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndinati, Adzeranji awa? Ndipo ananena, nati, Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, wopandanso wina woweramutsa mutu wake; koma awa anadza kuziopsa, kugwetsa nyanga za amitundu, amene anakwezera dziko la Yuda nyanga zao kulimwaza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinafunsa kuti, “Amisiri a zitsulowa akudzachita chiyani?” Iye anayankha kuti, “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda kotero kuti panalibe wina amene akanalimbana nazo, koma amisiri a zitsulowa abwera kudzaziopseza ndi kugwetsa nyanga zimenezi za mitundu ya anthu amene analimbana ndi dziko la Yuda ndi kubalalitsa anthu ake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndinati, Adzeranji awa? Ndipo ananena, nati, Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, wopandanso wina woweramutsa mutu wace; koma awa anadza kuziopsa, kugwetsa nyanga za amitundu, amene anakwezera dziko la Yuda nyanga zao kulimwaza.