Zechariah 1:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musakhale ngati makolo anu, amene adamva mau a aneneri akale ofotokoza uthenga wanga wakuti, ‘Lekani makhalidwe anu oipa ndi ntchito zanu zoipa.’ Koma iwowo sadamve kapena kulabadako, akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamakhala ngati makolo anu, amene aneneri akale anawafuulira, ndi kuti, Atero Yehova wa makamu Bwereranitu kuleka njira zanu zoipa, ndi machitidwe anu oipa; koma sanamve, kapena kumvera Ine ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musakhale ngati makolo anu, amene aneneri akale anawalalikira kuti: Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Tsopano lekani njira zanu zoyipa ndi machitidwe anu oyipawo.’ Koma iwo sanamvere kapena kulabadira za Ine, akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamakhala ngati makolo anu, amenie aneneri akale anawapfuulira, nd kuti, Atero Yehova wa makamu Bwereranitu kuleka njira zanu zoipa, ndi macitidwe anu oipa; ko ma sanamva, kapena klimvera Ine ati Yehova.