Zechariah 1:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi mau anga ndi malamulo anga amene ndidauza atumiki anga aneneri, suja adamveka kwa makolo anu? Choncho iwo adalapa ndi kunena kuti, ‘Chauta Wamphamvuzonse watichitadi zomwe adaatsimikiza kuti adzatichita, potsata makhalidwe athu ndi ntchito zathu zoipa.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi mawu anga ndi malangizo anga, amene ndinawawuza atumiki anga aneneri, suja anawachitira makolo anu? “Tsono iwo analapa ndi kunena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse watichitira zomwe zikuyenera njira zathu ndi machitidwe athu, monga anatsimikiza kuti adzachita.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeza makolo anu? ndipo anabwera, nati, Monga wno Yehova wa makamu analingirira kuticitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa macitidwe athu, momwemo anaticitira. Masomphenya oyamba: akavalo,