Zechariah 1:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Usiku wathawu ndinaona zinthu m'masomphenya. Ndinaona munthu atakwera pa kavalo wofiira. Munthuyo anaima pa timitengo tazitsamba m'chigwa. Kumbuyo kwake kunalinso akavalo, ena ofiira, ena odera, ena oyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinaona usiku, taonani, munthu woyenda pa kavalo wofiira, alikuima pakati pa mitengo yamchisu inali kunsi; ndi pambuyo pake panali akavalo ofiira, odera ndi oyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi ya usiku ndinaona masomphenya. Ndinaona munthu atakwera pa kavalo wofiira. Iye anayima pakati pa mitengo ya mchisu mʼchigwa. Kumbuyo kwake kunali akavalo ofiira, akhofi ndi oyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinaona usiku, taonani, munthu woyenda pa kavalo wofiira, alikuima pakati pa mitengo yamcisu inali kunsi; ndi pambuyo pace panali akavalo ofiira, odera ndi oyera.