Zechariah 10:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pemphani Chauta kuti akupatseni mvula pa nyengo yobzala. Ndiye amene amapanga mitambo yamvula. Ndiye amene amagwetsera anthu mvula yamvumbi, ndiye amene amameretsera aliyense mbeu m'munda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pemphani kwa Yehova mvula, m'nyengo ya mvula ya masika, kwa Yehova wolenga mphezi; ndipo adzawapatsa mivumbi ya mvula, kwa yense zophukira kuthengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pemphani mvula kwa Yehova pa nthawi yamphukira; ndi Yehova amene amapanga mitambo ya mvula. Iye amagwetsa mivumbi ya mvula kwa anthu, ndi kumeretsa mbewu za mʼmunda kwa aliyense.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pemphani kwa Yehova mvula, m'nyengo ya mvula ya masika, kwa Yehova wolenga mphezi; ndipo adzawapatsa mibvumbi ya mvula, kwayense zophukira kuthengo.