Zechariah 10:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene azidzaoloka nyanja ya ku Ejipito, ndidzathetsa mafunde a pa nyanjayo, madzi onse a mtsinje wa Nailo adzaphweratu. Kudzikuza kwa Asiriya kudzatha, ndipo ndodo yaufumu ya Ejipito idzathyoka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m'nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asiriya kudzagwetsedwa; ndi ndodo yachifumu ya Ejipito idzachoka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzawoloka nyanja ya masautso; nyanja yokokoma idzagonja ndipo madzi onse a mu Nailo adzaphwa. Kudzikuza kwa Asiriya kudzatha ndipo ndodo yaufumu ya Igupto idzathyoka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzapita pakati pa nyanja ya nsautso, nadzapanda mafunde a m'nyanja, ndi maiwe onse a mtsinje adzaphwa; ndi kudzikuza kwa Asuri kudzagwetsedwa; ndi ndodo yacifumu ya Aigupto idzacoka.