Zechariah 10:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja mafano am'nyumba amalankhula zonama, ndipo oombeza maula amaona zabodza. Olota maloto amalota zabodza, ndipo mau ao othuzitsa mtima ndi nkhambakamwa chabe. Motero anthu amangoyenda uku ndi uku ngati nkhosa, amazunzika chifukwa chosoŵa mbusa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti aterafi anena zopanda pake, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto achabe, asangalatsa nazo zopanda pake; chifukwa chake ayendayenda ngati nkhosa, azunzika popeza palibe mbusa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafano amayankhula zachinyengo, owombeza mawula amaona masomphenya abodza; amafotokoza maloto onama, amapereka chitonthozo chopandapake. Choncho anthu amangoyendayenda ngati nkhosa zozunzika chifukwa chosowa mʼbusa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti aterafi anena zopanda pace, ndi aula aona bodza; nafotokoza maloto acabe, asangalatsa nazo zopanda pace; cifukwa cace ayendayenda ngati nkhosa, azunzika popeza palibe mbusa.