Zechariah 10:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Ndaŵakwiyira kwambiri abusa, ndipo atsogoleri a m'dzikomo ndidzaŵalanga. Koma Ine Chauta Wamphamvuzonse ndidzasamala nkhosa zanga, ndiye kuti banja la Yuda, ndipo ndidzazisandutsa ngati akavalo ankhondo amphamvu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mkwiyo wanga wayakira abusa, ndipo ndidzalanga atonde; pakuti Yehova wa makamu adzazonda zoweta zake, ndizo nyumba ya Yuda, nadzaziika ngati kavalo wake waulemerero kunkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine ndawakwiyira kwambiri abusa, ndipo ndidzalanga atsogoleri; pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzasamalira nkhosa zake, nyumba ya Yuda, ndi kuwasandutsa ngati akavalo aulemerero ankhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mkwiyo wanga wayakira abusa, ndipo ndidzalanga atonde; pakuti Yehova wa makamu adzazonda zoweta zace, ndizo nyumba ya Yuda, nadzaziika ngati kavalo wace waulemerero kunkhondo.