Zechariah 10:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Banja la Yuda ndidzalilimbitsa, banja la Yosefe ndidzalipambanitsa. Anthuwo ndidzaŵabwezanso kwao chifukwa choti ndaŵamvera chifundo. Tsono adzakhala ngati kuti sindidaŵataye, pakuti Ine ndine Chauta, Mulungu wao, ndipo ndidzayankha zopempha zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataya konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda ndi kupulumutsa nyumba ya Yosefe. Ndidzawabwezeretsa chifukwa ndawamvera chisoni. Adzakhala ngati kuti sindinawakane, chifukwa ndine Yehova Mulungu wawo ndipo ndidzawayankha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawacitira cifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataya konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera.