Zechariah 10:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Aefuremu adzakhala ngati ankhondo amphamvu, adzasangalala ngati anthu okhuta vinyo. Ana ao adzaziwona zimenezi, nawonso nkusangalala, mumtima mwao mudzadzaza chimwemwe, chifukwa cha zimene Chauta wachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo a ku Efuremu adzakhala ngati ngwazi, ndi mtima wao udzakondwera ngati ndi vinyo; ndipo ana ao adzachiona nadzakondwera; mtima wao udzakondwerera mwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aefereimu adzakhala ngati ankhondo amphamvu adzasangalala ngati anthu amene amwa vinyo. Ana awo adzaziona zimenezi ndipo adzasangalala; mʼmitima mwawo adzakondwa mwa Ambuye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo a ku Efraimu adzakhala ngati ngwazi, ndi mtima wao udzakondwera ngati ndi vinyo; ndipo ana ao adzaciona nadzakondwera; mtima wao udzakondwerera mwa Yehova.