Zechariah 10:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidzaliza mluzu kuti anthu anga asonkhane pamodzi. Ndidaŵapulumutsa, ndipo adzachuluka monga momwe adaaliri masiku amakedzana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzawaimbira mluzu ndi kuwasonkhanitsa, pakuti ndawaombola; ndipo adzachuluka monga anachulukira kale.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzaliza mluzu ndi kuwasonkhanitsa pamodzi. Ndithu ndawawombola; adzachulukana ngati poyamba paja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzawayimbira mluzu ndi kuwasonkhanitsa, pakuti ndawaombola; ndipo adzacuruka monga anacurukira kale.