Zechariah 11:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono eni nkhosawo ndidaŵauza kuti “Ngati zakukomerani, mundilipire. Koma ngati si choncho, sungani ndalama zanu.” Ndiye iwowo adandilipira masekeli asiliva makumi atatu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinanena nao, Chikakomera inu, ndipatseni mphotho yanga; ngati iai, lekani. Ndipo anayesa mphotho yanga, kulemera kwake masekeli a siliva makumi atatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinawawuza kuti, “Ngati mukuganiza kuti zili bwino, patseni malipiro anga; koma ngati si choncho, sungani malipirowo.” Kotero anandipatsa ndalama zasiliva makumi atatu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinanena nao, Cikakomera inu, ndipatseni mphotho yanga; ngati iai, lekani. Ndipo anayesa mphotho yanga, kulemera kwace ndarama zasiliva makumi atatu.