Zechariah 11:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Uziponye mosungira chuma.” Motero ndidatenga masekeli asiliva zija, mtengo uja adaati ndiyenera kulandirawu, nkukaziponya mosungira chuma m'Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa ine, Kaziponye kwa woumba mbiya, mtengo wake wokometsetsa anandiyesawo. Ndipo ndinatenga masekeli makumi atatu a siliva, ndi kuziponya kwa woumba mbiya, m'nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ziponye kwa wowumba mbiya,” mtengo woyenera umene anapereka pondigula Ine! Choncho ndinatenga ndalama zasiliva makumi atatu ndi kuziponya mʼnyumba ya Yehova kwa wowumba mbiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa ine, Kaziponye kwa woumba mbiya, mtengo wace wokometsetsa anandiyesawo. Ndipo ndinatenga ndarama makumi atatu asiliva, ndi kuziponya kwa woumba mbiya, m'nyumba ya Yehova.