Zechariah 11:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti ndidzakuika mbusa m'dziko, mbusa amene sadzasamala nkhosa zotayika, sadzanka nafunafuna zosokera, kapena kuchiritsa zopunduka, ndi kudyetsa zamoyo. Koma iye azidzangodya nyama ya nkhosa zonona, mpaka kumapulula ndi ziboda zake zomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti taonani, ndidzautsa mbusa m'dziko amene sadzazonda otayika, kapena kufunafuna zomwazika, kapena kulunzitsa yothyoka, kapena kudyetsa yamoyo, koma adzadya nyama ya zonenepa, nadzang'amba ziboda zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ndidzawutsa mʼbusa mʼdzikomo amene sadzasamalira zotayika, kapena kufunafuna zazingʼono, kapena zovulala, kapena kudyetsa nkhosa zabwino, koma iye adzadya nyama ya nkhosa zonenepa, nʼkumakukuta ndi ziboda zomwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti taonani, ndidzautsa mbusa m'dziko amene sadzazonda otayika, kapena kufunafuna zomwazika, kapena kulunzitsa yotyoka, kapena kudyetsa yamoyo, koma adzadya nyama ya zonenepa, nadzang'amba ziboda zao.