Zechariah 11:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lirani mokweza, inu mitengo ya paini, pakuti mikungudza yagwa, mitengo yamphamvu yaonongeka. Lirani mokweza inu mitengo ya thundu ya ku Basani, pakuti nkhalango yoŵirira ija aiyeretsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chema, mtengo wamlombwa, pakuti mkungudza wagwa, popeza mitengo yokoma yaipitsidwa; chemani athundu a ku Basani, pakuti nkhalango yotchinjirizika yagwa pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lira mwachisoni, iwe mtengo wa payini, pakuti mkungudza wagwa; mtengo wamphamvu wawonongeka! Lirani mwachisoni, inu mitengo ya thundu ya Basani; nkhalango yowirira yadulidwa!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cema, mtengo wamlombwa, pakuti mkungudza wagwa, popeza mitengo yokoma yaipitsidwa; cemani athundu a ku Basani, pakuti nkhalango yocinjirizika yagwa pansi.