Zechariah 11:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imvani abusa, nawonso akulira mokweza, pakuti mabusa ao obiriŵira auma. Imvani misona ya mikango ikubangula, pakuti nkhalango yoŵirira ya ku Yordani aiyeretsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mau a kuchema kwa abusa! Pakuti ulemerero wao waipsidwa; mau a kubangula kwa misona ya mikango! Pakuti kudzikuza kwa Yordani kwaipsidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Imvani kulira mwachisoni kwa abusa; msipu wawo wobiriwira wawonongeka! Imvani kubangula kwa mikango; nkhalango yowirira ya ku Yorodani yawonongeka!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mau a kucema kwa abusa! pakuti ulemerero wao waipsidwa; mau a kubangula kwa misona ya mikango! pakuti kudzikuza kwa Yordano kwaipsidwa.