Zechariah 11:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene amagula nkhosa amazipha, koma salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Atamandike Chauta, ine ndalemera!’ Ndipo abusa ake sadzazimvera chifundo nkhosazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
zimene eni ake azipha, nadziyesera osapalamula; ndi iwo akuwagulitsa akuti, Alemekezedwe Yehova, pakuti ine ndine wolemera; ndi abusa ao sazichitira chifundo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amene amagula nkhosazo amazipha ndipo salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Alemekezeke Yehova, ine ndalemera!’ Abusa ake omwe sazimvera chisoni nkhosazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
zimene eni ace azipha, nadziyesera osaparamula; ndi iwo akuwagulitsa akuti, Alemekezedwe Yehova, pakuti ine ndine wolemera; ndi abusa ao sazicitira cifundo.