Zechariah 11:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho onse okhala m'dziko lapansi, sindidzaŵamveranso chifundo. Ndikutero Ine Chauta. Munthu aliyense ndidzampereka m'manja mwa mtsogoleri wake ndi mwa mfumu yake. Ndipo iwowo adzasakaza dziko lonse, koma Ine sindidzampulumutsa aliyense m'manja mwao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sindidzachitiranso chifundo okhala m'dzikomo, ati Yehova; koma taonani, ndidzapereka anthu, yense m'dzanja la mnansi wake, ndi m'dzanja la mfumu yake; ndipo iwo adzakantha dzikoli, ndi m'dzanja mwao sindidzawalanditsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Ine sindidzamveranso chisoni anthu okhala mʼdziko,” akutero Yehova. “Ndidzapereka munthu aliyense mʼmanja mwa mnansi wake ndi mwa mfumu yake. Iwo adzazunza dziko, ndipo Ine sindidzawapulumutsa mʼmanja mwawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sindidzacitiranso cifundo okhala m'dzikomo, ati Yehova; koma taonani, ndidzapereka anthu, yense m'dzanja la mnansi wace, ndi m'dzanja la mfumu yace; ndipo iwo adzakantha dzikoli, ndi m'dzanja mwao sindidzawalanditsa.