Zechariah 11:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ine ndidayamba kuŵeta nkhosa zokaphedwa zija. Ndidatenga ndodo ziŵiri: yoyamba ndidaitcha dzina lakuti “Kukoma mtima”, yachiŵiri ndidaitcha “Umodzi.” Tsono gulu la nkhosa lija ndidaliŵetadi bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mwemo ndinadyetsa zoweta zakukaphedwa, ndizo zoweta zonyankhalala. Ndipo ndinadzitengera ndodo ziwiri; ina ndinaitcha Chisomo, inzake ndinaitcha Chomanganitsa; ndipo ndinadyetsa zowetazo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ine ndinadyetsa nkhosa zokaphedwa, makamaka nkhosa zoponderezedwa. Pamenepo ndinatenga ndodo ziwiri ndipo yoyamba ndinayitcha Kukoma mtima ndipo yachiwiri ndinayitcha Umodzi ndipo ndinadyetsa nkhosazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mwemo ndinadyetsa zoweta zakukaphedwa, ndizo zoweta zonyankhalala. Ndipo ndinadzitengera ndodo ziwiri; yina ndinaicha Cisomo, inzace ndinaicha Comanganitsa; ndipo ndinadyetsa zowetazo.