Zechariah 12:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mau a Chauta onena za Israele. Chauta ndiye adayala mlengalenga ndi kukhazikitsa dziko lapansi, ndiyenso amene adalenga mpweya wokhala mwa munthu. Iye akunena kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Katundu wa mau a Yehova wakunena Israele. Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m'kati mwake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uthenga wa Yehova kwa Israeli. Yehova, amene amayala mlengalenga, amene amayika maziko a dziko lapansi, ndiponso amene amalenga mzimu wokhala mwa munthu, akunena kuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Katundu wa mau a Yehova wakunena Israyeli. Atero Yehova, wakuyala miyamba, ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kulenga mzimu wa munthu m'kati mwace;