Zechariah 12:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono anthu a pa banja la Davide ndi anthu onse a ku Yerusalemu ndidzaŵadzaza ndi mtima wachifundo ndi wakupemphera. Motero adzati atamuyang'ana amene adambaya, adzamlira kwabasi monga muja amamlirira mwana akakhala mmodzi yekha. Adzamliradi kwambiri monga muja amamlirira mwana wachisambamu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala m'Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo pa nyumba ya Davide ndi pa anthu okhala mu Yerusalemu ndidzakhuthulirapo mzimu wachisomo ndi wopemphera. Iwo adzandiyangʼana Ine, amene anamubaya, ndipo adzamulirira kwambiri monga momwe munthu amalirira mwana wake mmodzi yekhayo, ndiponso adzamva chisoni kwambiri monga momwe amachitira ndi mwana woyamba kubadwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala m'Yerusalemu, mzimu wa cisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wace mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wace woyamba.