Zechariah 12:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidzasandutsa Yerusalemu kuti akhale ngati chikho cha vinyo amene adzasokoneza mitundu yonse ya anthu yomzungulira. Adani omwewo adzathira nkhondo dziko la Yuda ndiponso mzinda wa Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, ndidzaika Yerusalemu akhale chipanda chodzandiritsa kwa mitundu yonse ya anthu yozungulirapo, ndipo chidzafikira Yuda yemwe pomangira misasa Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Taonani, ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala chakumwa choledzeretsa chimene chidzasokoneza mitundu yonse ya anthu yomuzungulira. Yuda adzazingidwa pamodzinso ndi Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, ndidzaika Yerusalemu akhale cipanda codzandiritsa kwa mitundu yonse ya anthu yozungulirapo, ndipo cidzafikira Yuda yemwe pomangira misasa Yerusalemu.