Zechariah 12:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo Yerusalemu ndidzamsandutsa mwala wolemera kwambiri kwa mitundu yonse ya anthu. Onse oyesa kuunyamula, udzaŵapweteka koopsa. Mitundu yonse ya anthu a pansi pano idzasonkhana pamodzi kuti imuukire Yerusalemu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndi amitundu onse a pa dziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku limenelo, pamene mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi idzasonkhana kulimbana naye, ndidzasandutsa Yerusalemu thanthwe losatheka kusunthidwa ndi mitundu yonse ya anthu. Onse oyesa kumusuntha adzadzipweteka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzacitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndi amitundu onse a pa dziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao.