Zechariah 12:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Tsiku limenelo kavalo aliyense ndidzamchititsa mantha osokonezeka nawo, ndipo wokwerapo wake adzachita msala. Banja la Yuda ndidzaliyang'anira, koma akavalo a adani ao onse ndidzaŵachititsa khungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzakantha kavalo aliyense ndi kumdabwitsa, ndi womkwera adzayaluka; ndipo ndidzatsegulira maso anga nyumba ya Yuda, ndi kukantha kavalo aliyense wa mitundu ya anthu akhale wakhungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku limenelo kavalo aliyense ndidzamuchititsa mantha kuti asokonezeke, ndipo wokwerapo wake ndidzamuchititsa misala,” akutero Yehova. “Ndidzayangʼanira nyumba ya Yuda koma ndidzachititsa khungu akavalo onse a anthu a mitundu ina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzakantha kavalo ali yense ndi kumdabwitsa, ndi womkwera adzayaluka; ndipo ndidzatsegulira maso anga nyumba ya Yuda, ndi kukantha kavalo ali yense wa mitundu ya anthu akhale wakhungu.