Zechariah 12:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo mafuko a ku Yuda ndidzaŵasandutsa ngati mbaula yotentha pakati pa nkhuni, ngati nsakali yoyaka pakati pa mitolo ya tirigu. Adzatentha mitundu yonse ya anthu yoŵazungulira, kumanja ndi kumanzere, koma anthu a ku Yerusalemu adzakhalabe mwamtendere mumzinda mwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, kudzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwake, m'Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pa tsiku limenelo ndidzasandutsa atsogoleri a Yuda kukhala ngati mbawula yotentha pakati pa nkhuni, ngati sakali yoyaka pa mitolo ya tirigu. Adzatentha mitundu yonse ya anthu yowazungulira, kumanja ndi kumanzere, koma Yerusalemu sadzasuntha pa malo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, ku dzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwace, m'Yerusalemu.