Zechariah 12:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo Chauta adzakhala ngati chishango chotchinjiriza anthu a ku Yerusalemu, kotero kuti anthu ofooka kwambiri mwa iwo adzakhala amphamvu ngati mfumu Davide. Tsono banja la Davide lidzakhala lolamulira zonse ngati Mulungu, ngati mngelo wa Chauta woŵatsogolera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku ilo Yehova adzatchinjiriza okhala m'Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku limenelo Yehova adzatchinjiriza onse okhala mu Yerusalemu, kotero kuti anthu ofowoka kwambiri pakati pawo adzakhala ngati Davide, ndipo nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mngelo wa Yehova wowatsogolera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku ilo Yehova adzacinjiriza okhala m'Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao.