Zechariah 13:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wina aliyense akadzafunabe kuti azilosa, bambo wake ndi mai wake adzamuuza kuti, ‘Sudzakhalanso ndi moyo chifukwa choti ukulosa zabodza m'dzina la Chauta.’ Motero makolo ake omwe adzambaya pamene munthuyo akulosa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzachitika, akaneneranso wina, atate wake ndi mai wake ombala adzanena naye, Sudzakhala ndi moyo, pakuti unena bodza m'dzina la Yehova; ndipo atate wake ndi mai wake ombala adzamgwaza ponenera iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati wina aliyense adzafuna kunenera, abambo ndi amayi ake amene anamubereka, adzamuwuza kuti, ‘Uyenera kufa, chifukwa wayankhula bodza mʼdzina la Yehova.’ Pamene anenera, makolo ake omwe adzamubaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzacitika, akaneneranso wina, atate wace ndi mai wace ombala adzanena naye, Sudzakhala ndi moyo, pakuti unena bodza m'dzina la Yehova; ndipo atate wace ndi mai wace ombala adzamgwaza ponenera iye.