Zechariah 13:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha zinthu zimene akuti amaziwona m'masomphenya pamene akulosa. Sadzavalanso mwinjiro wake waubweya woti azinamizira anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo kuti aneneri adzachita manyazi yense ndi masomphenya ake, ponenera iye; ndipo sadzavala chofunda chaubweya kunyenga nacho;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pa tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha masomphenya ake. Sadzavala chovala chake chaubweya ndi cholinga chonamiza anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo kuti aneneri adzacita manyazi yense ndi masomphenya ace, ponenera iye; ndipo sadzabvala copfunda caubweya kunyenga naco;