Zechariah 13:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo wina akadzafunsa kuti, ‘Nanga zilonda zili kumsana kwakozi, udatani?’ Iye adzati, ‘Zilondazi ndidazilandira m'nyumba mwa abwenzi anga.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wina akati kwa iye, Zipsera izi m'manja mwako nza chiyani? Adzayankha, Ndizo za mabala anandilasa m'nyumba ya ondikonda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wina adzamufunsa, ‘Zilonda zili mʼthupi lakoli ndi chiyani?’ Iye adzayankha kuti, ‘Zilondazi ndinazilandira mʼnyumba ya abwenzi anga.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wina akati kwa iye, Zipsera izi m'manja mwako nza ciani? adzayankha, Ndizo za mabala anandilasa m'nyumba ya ondikonda.