Zechariah 13:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Lupanga iwe, dzambatuka, ukanthe mbusa wanga. Ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine. Ndikutero Chauta Wamphamvuzonse. Kantha mbusa kuti nkhosa zimwazikane. Pamenepo ndidzakantha ndi anthu wamba omwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Dzambatuka iwe lupanga, ukanthe mʼbusa wanga, ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine!” akutero Yehova Wamphamvuzonse. Kantha mʼbusa ndipo nkhosa zidzabalalika, ndipo ndidzatambalitsa dzanja langa kuwononga zazingʼono.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.