Zechariah 13:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akuti, “Mwa zigawo zitatu za anthu m'dziko monsemo ziŵiri zidzaphedwa, chidzangokhalako chigawo chimodzi chokha chamoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzachitika m'dziko lonse, ati Yehova, magawo awiri m'menemo adzalikhidwa nadzafa; koma gawo lachitatu lidzasiyidwa m'mwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼdziko monse, akutero Yehova Wamphamvuzonse, “zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za anthu zidzakanthidwa ndi kuwonongeka; koma chigawo chimodzi chidzatsala mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzacitika m'dziko lonse, ati Yehova, magawo awiri m'menemo adzalikhidwa nadzafa; koma gawo lacitatu lidzasiyidwa m'mwemo.