Zechariah 14:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko lonse adzalisalaza kuyambira ku Geba mpaka ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu. Koma Yerusalemu adzakwezedwa pamalo pakepo, kuyambira ku chipata cha Benjamini mpaka ku malo amene kunali chipata chakale mpaka ku chipata chapangodya, ndiponso kuchokera ku Nsanja ya Hananele mpaka ku malo opondera mphesa za mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga chidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwera kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m'malo mwake, kuyambira ku chipata cha Benjamini kufikira ku malo a chipata choyamba, kufikira ku chipata cha kungodya, ndi kuyambira nsanja ya Hananele kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko lonse, kuyambira ku Geba mpaka ku Rimoni, kummwera kwa Yerusalemu, lidzakhala ngati Araba. Koma Yerusalemu adzakwezedwa ndipo adzakhala pamalo pakepo, kuyambira ku Chipata cha Benjamini mpaka ku malo amene ali ku Chipata Choyamba, ku Chipata Chapangodya, ndipo kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku malo opsinyira mphesa za mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dziko lonse lidzasandulika, lidzanga cidikha, kuyambira ku Geba kufikira ku Rimoni, kumwela kwa Yerusalemu; ndipo pali uwupo padzakhala ponyamuka, ndipo udzakhala m'malo mwace, kuyambira ku cipata ca Benjamini kufikira ku malo a cipata coyamba, kufikira ku cipata ca kungondya, ndi kuyambira nsanja ya Hananeli kufikira ku zoponderamo mphesa za mfumu.