Zechariah 14:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zitatha zimenezi anthu onse otsala mwa adani amene ankamenyana ndi Yerusalemu, azidzabwera chaka ndi chaka kudzapembedza Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse, ndiponso kudzachita chikondwerero chamisasa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzachitika kuti otsala onse a amitundu onse anadzawo kulimbana ndi Yerusalemu, adzakwera chaka ndi chaka kulambira mfumu Yehova wa makamu, ndi kusunga chikondwerero cha Misasa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka opulumuka ochokera mwa mitundu yonse ya anthu amene anathira nkhondo Yerusalemu, azidzapita chaka ndi chaka kukapembedza Mfumu Yehova Wamphamvuzonse, ndiponso kukachita Chikondwerero cha Misasa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzacitika kuti otsala onse a amitundu onse anadzawo kulimbana ndi Yerusalemu, adzakwera caka ndi caka kulambira mfumu Yehova wa makamu, ndi kusunga madyerero amisasa.