Zechariah 14:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati anthu a ku Ejipito sadzapita kukaonekera kumeneko, adzalandiranso chilango chonga chomwe Chauta adzalange nacho mtundu wina uliwonse wa anthu osapita kukachita chikondwerero chamisasa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo banja la ku Ejipito likapanda kukwera, losafika, sudzawagwera kodi mliri umene Yehova adzakantha nao amitundu osakwera kusunga chikondwerero cha Misasa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati anthu a ku Igupto sadzapita ndi kukakhala nawo kumeneko, adzakhala wopanda mvula. Yehova adzabweretsa pa iwo mliri umene analangira mitundu ina ya anthu imene sinapite ku Chikondwerero cha Misasa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo banja la ku Aigupto likapanda kukwera, losafika, sirdzawagwera kodi mliri umene Yehova adzakantha nao amitundu osakwera kusunga madyerero amisasa?