Zechariah 14:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu. Adzaulanda mzindawo ndi kuphwasula nyumba zonse, ndipo akazi am'menemo adzaŵachita chigololo. Theka la anthu a mu mzindawo lidzatengedwa ukapolo, koma ena onse otsala mumzindamo sadzachotsedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndidzasonkhanitsa amitundu onse alimbane ndi Yerusalemu; ndipo mudziwo udzalandidwa, ndi nyumba zidzafunkhidwa, ndi akazi adzakakamizidwa; ndi limodzi la magawo awiri la mudzi lidzatuluka kunka kundende, koma anthu otsala sadzaonongeka m'mudzimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu; mzindawu udzalandidwa, nyumba zidzaphwasulidwa, ndipo akazi adzagwiriridwa. Theka la anthu a mu mzindamu lidzapita ku ukapolo, koma ena onse otsala mu mzindamu sadzachotsedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndidzasonkhanitsa amitundu onse alimbane ndi Yerusalemu; ndipo mudziwo udzalandidwa, ndi nyumba zidzafunkhidwa, ndi akazi adzakakamizidwa; ndi limodzi la magawo awiri la mudzi lidzaturuka kumka kundende, koma anthu otsala sadzaonongeka m'mudzimo.