Zechariah 14:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku limenelo pa mabelu ovala akavalo ankhondo padzalembedwa mau akuti, “Woperekedwa kwa Chauta.” Ndipo mbiya za ku Nyumba ya Chauta nazonso zidzakhala zoyera ngati mbale zakuguwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku lomwelo padzaoneka pa miliu ya akavalo Opatulikira Yehova; ndi mbiya za m'nyumba ya Yehova zidzanga mbale za kuguwa la nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku limenelo pa maberu a akavalo padzalembedwa mawu oti WOPATULIKIRA YEHOVA, ndipo miphika ya mʼNyumba ya Yehova idzakhala yopatulika ngati mbale za ku guwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku lomwelo padzaoneka pa miriu ya akavalo OPATULIKIRA YEHOVA; ndi mbiya za m'nyumba ya Yehova zidzanga mbale za ku guwa la nsembe.