Zechariah 14:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo adzaimirira pa phiri la Olivi loyang'anana ndi Yerusalemu chakuvuma, ndipo phirilo lidzagaŵika paŵiri ndi chigwa chachikulu choyenda kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. Theka la phiri lidzasunthira chakumpoto, theka lina chakumwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mapazi ake adzaponda tsiku lomwelo pa phiri la Azitona, lili pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala chigwa chachikulu; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo adzayimirira pa Phiri la Olivi, kummawa kwa Yerusalemu, ndipo Phiri la Olivilo lidzagawikana pawiri kuyambira kummawa mpaka kumadzulo, kupanga chigwa chachikulu, kuchititsa kuti theka la phiri lisunthire kumpoto ndi linalo kummwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mapazi ace adzaponda tsiku lomwelo pa phiri la Azitona, liri pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala cigwa cacikuru; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwela.